YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 31

31
Afafaniza chipembedzo chonse cha mafano
1 # 2Maf. 18.4 Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumidzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efuremunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumidzi yao.
2 # 1Mbi. 23.6, 30-31 Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Ambuye. 3Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova. 4#Num. 18.8-24; Neh. 13.10, 12Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'chilamulo cha Yehova. 5Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka. 6#Lev. 27.30, 32Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu. 7Mwezi wachitatu anayamba kuika miyalo ya miyuluyi, naitsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. 8Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele. 9Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuluyi. 10#Mala. 3.10Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala. 11Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza. 12Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye. 13Ndi Yehiyele, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asahele, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyele, ndi Isimakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wake, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkulu wa kunyumba ya Mulungu. 14Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri. 15Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Miniyamini, ndi Yesuwa, ndi Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akulu monga ang'ono; 16pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao; 17#1Mbi. 23.24, 27ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao; 18ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ana ao ang'ono onse, akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m'kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika; 19#Lev. 25.34panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao. 20#2Maf. 18.3Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.

Currently Selected:

2 MBIRI 31: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in