2 MBIRI 24
24
Yowasi akonzanso Kachisi
1 #
2Maf. 11.21—12.15
Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la make ndiye Zibiya wa ku Beereseba. 2Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe. 3Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi. 4Ndipo pambuyo pake mumtima mwa Yowasi munali chofuna kukonzanso nyumba ya Yehova. 5Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumidzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo. 6Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni? 7Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala. 8Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja kuchipata cha nyumba ya Yehova. 9Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisraele m'chipululu. 10Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha. 11Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka. 12Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova. 13Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa. 14Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
Anthu apatukira mafano
15Koma Yehoyada anakalamba, nachuluka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira. 16Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino m'Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake. 17Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera. 18#Ower. 5.8Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene. 19#Yer. 7.25-26Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawachitira umboni; koma sanawamvere.
Zekariya adzudzula anthu naphedwa
20 #
Num. 14.41; 2Mbi. 15.2 Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu. 21#Mat. 23.35; Mac. 7.58-59Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova. 22Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse. 23#2Maf. 12.17-18Ndipo kunachitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko. 24Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga. 25Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu. 26Omchitira chiwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi Mwamoni; ndi Yehozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmowabu. 27Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Currently Selected:
2 MBIRI 24: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi