2 MBIRI 25
25
Amaziya agonjetsa Aedomu
1 #
2Maf. 14.1-6
Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu. 2Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro. 3Kunachitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ake amene adapha mfumu atate wake. 4Koma sanaphe ana ao, koma anachita monga umo mulembedwa m'chilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere tchimo lakelake. 5Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa. 6Analemberanso ngwazi zamphamvu za m'Israele zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente a siliva zana limodzi. 7Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu. 8Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa. 9#Miy. 10.22Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani. 10Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kuchokera ku Efuremu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima. 11#2Maf. 14.7Nalimbika mtima Amaziya. Natsogolera anthu ake, namuka ku Chigwa cha Mchere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi. 12Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo. 13Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betehoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.
Amaziya alangidwa popembedza mafano
14Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira. 15#Mas. 96.5Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu? 16Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.
17 #
2Maf. 14.8-14
Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani, tionane maso. 18#Ower. 9.8Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi. 19Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu. 20#1Maf. 12.15Koma wosamvera Amaziya, pakuti ncha Mulungu ichi kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu. 21Motero anakwera Yowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda. 22Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawa yense kuhema kwake. 23Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai. 24Natenga golide ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obededomu, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwerera kunka ku Samariya.
25 #
2Maf. 14.17-22
Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu. 26Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwa kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele? 27Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko. 28Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Yuda.
Currently Selected:
2 MBIRI 25: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi