YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 8

8
Aisraele akhumba mfumu
1Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake amuna akhale oweruza a Israele. 2Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba. 3#Eks. 18.21; 1Tim. 3.3; 1Tim. 6.10Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.
4Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama; 5#Deut. 17.14; Mac. 13.21nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo muchitidwa m'mitundu yonse ya anthu. 6Koma chimenechi sichinakondweretsa Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova. 7#Eks. 16.8; Hos. 13.10-11Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao. 8Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso. 9Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.
10Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova. 11#Deut. 17.14-20; 1Sam. 14.52Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake; 12idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta. 13Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate. 14#1Maf. 21.7Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mphesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake. 15Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake. 16Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake. 17Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake. 18Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo. 19#2Mbi. 24.19; Yer. 44.16Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu; 20#1Sam. 8.5; 2Maf. 17.15kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kutuluka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu. 21Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova. 22#1Sam. 8.7Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumudzi wake.

Currently Selected:

1 SAMUELE 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in