1 SAMUELE 7
7
1Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.
Afilisti akanthidwa ku Mizipa
2Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu m'Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova. 3#Deut. 30.2-10; 1Maf. 8.48-49; Yes. 55.7Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti. 4#Ower. 2.11Pomwepo ana a Israele anachotsa Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.
5Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova. 6#Ower. 20.1-2; 2Sam. 23.16Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele m'Mizipa. 7Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo. 8#Yes. 37.4Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo. 9#Mas. 99.6Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza. 10#2Sam. 22.14-15Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele. 11Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara. 12#Gen. 28.18Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza. 13#Ower. 13.1Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele. 14Ndipo midzi ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa milaga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere; 15#1Sam. 7.6ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake. 16Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa. 17Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.
Currently Selected:
1 SAMUELE 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi