YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 28

28
Saulo afunsira mkazi wobwebweta ku Endori
1Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako. 2Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.
3 # Lev. 19.31; 1Sam. 28.9 M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika m'Rama, m'mudzi mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse. 4#1Sam. 31.1Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa. 5Ndipo pamene Saulo anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu. 6#1Sam. 14.37; Miy. 1.28Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri. 7Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta. 8#1Mbi. 10.13; Yes. 8.19Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake. 9#1Sam. 28.3Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa. 10Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi. 11Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samuele. 12Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau akulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo. 13Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko. 14#1Sam. 15.27Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira. 15#1Sam. 28.6Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita. 16Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako? 17Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide. 18#1Sam. 15.9; 1Mbi. 10.13Chifukwa sunamvera mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wake woopsa pa Amaleke, chifukwa chake Yehova wakuchitira chinthu ichi lero. 19Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti. 20Pomwepo Saulo anagwa pansi tantha, naopa kwakukulu, chifukwa cha mau a Samuele; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wake wonse anakhala osadya kanthu. 21Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine. 22Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka. 23Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama. 24Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa; 25nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo.

Currently Selected:

1 SAMUELE 28: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in