YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 27

27
1Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake. 2#1Sam. 21.10Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati. 3Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala. 4Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso.
5Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumilaga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wachifumu pamodzi ndi inu? 6Ndipo Akisi anampatsa Zikilagi tsiku lomweli; chifukwa chake Zikilagi ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.
7Ndipo kuwerenga kwake kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko chaka chimodzi ndi miyezi inai. 8Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito. 9Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi ngamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi. 10#Ower. 1.16Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni. 11Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti. 12Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.

Currently Selected:

1 SAMUELE 27: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in