YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 24

24
Davide aleka Saulo osamupha
1Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi. 2Tsono Saulo anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisraele onse, namuka, kukafuna Davide ndi anthu ake m'matanthwe a zinkhoma. 3Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo. 4Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika. 5#2Sam. 24.10Ndipo kunali m'tsogolo mwake kuti mtima wa Davide unamtsutsa chifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo. 6#1Sam. 26.11Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. 7#Mat. 5.44; Aro. 12.17, 19Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake. 8Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira. 9#Miy. 16.28; 17.9Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa. 10Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. 11#1Sam. 26.20; Mas. 7.3; 35.7Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire. 12#Gen. 16.5; Ower. 11.27; Yob. 5.8Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu. 13Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu. 14#1Sam. 17.43Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe. 15#1Sam. 24.12Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu. 16#1Sam. 26.17Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi. 17#Mat. 5.44Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa. 18#1Sam. 26.23Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandipha pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako. 19Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe. 20#1Sam. 23.17Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako. 21#2Sam. 21.6-8Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga. 22Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka.

Currently Selected:

1 SAMUELE 24: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in