YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 23

23
Davide alanditsa a ku Keila
1Tsono anauza Davide, kuti, Onani Afilisti alikuponyana ndi Keila, nafunkha za m'madwale. 2#2Sam. 5.19, 23Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila. 3Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti. 4Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako. 5Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.
6Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake. 7Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo. 8Ndipo Saulo anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ake. 9#Num. 27.21Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi. 10Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo chifukwa cha ine. 11Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika. 12Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka. 13Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.
Davide ndi Yonatani abwereza kupangana
14 # Mas. 11.1 Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lake. 15Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi. 16Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu. 17#1Sam. 24.20Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa. 18#1Sam. 18.3Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake. 19#1Sam. 26.1Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu? 20#Mas. 54.3Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu. 21Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo. 22Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu. 23Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda. 24Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu. 25Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni. 26#Mas. 17.9Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire. 27Koma mthenga unafika kwa Saulo ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yovumbulukira ya Afilisti yalowa m'dziko. 28Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa. 29Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m'ngaka za Engedi.

Currently Selected:

1 SAMUELE 23: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in