Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu. Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.