1 SAMUELE 25
25
Amwalira Samuele
1Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.
Za Davide, Nabala ndi Abigaile
2Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele. 3Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe. 4Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake. 5Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimele, mumuke kwa Nabala ndi kundiperekera moni; 6#1Mbi. 12.18; Luk. 10.5ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo. 7Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele. 8Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide. 9Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka. 10#Ower. 9.28Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Makono ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao. 11Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira? 12Chomwecho anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa. 13Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu. 14Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira. 15Koma anthu aja anatichitira zabwino ndithu, sanatichititse manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja; 16iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo. 17Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye. 18Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoochaocha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu. 19#Gen. 32.16, 20Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuyo mwanu. Koma sanauze mwamuna wake Nabala. 20Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa bulu wake, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ake analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao. 21#Miy. 17.13Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowa kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino. 22Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo. 23Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pa bulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira, 24Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu. 25Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaona anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza. 26#Gen. 20.6; 1Sam. 25.33; Aro. 12.19Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala. 27Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga. 28#2Sam. 7.11, 27Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse. 29Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala. 30Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele; 31mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu. 32Ndipo Davide anati kwa Abigaile, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; 33#Gen. 20.6; 1Sam. 25.6ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha. 34Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. 35#Luk. 7.50; 8.48Chomwecho Davide analandira m'dzanja lake zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndavomereza nkhope yako. 36Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutacha. 37Tsono m'mawa vinyo atamchokera Nabala, mkazi wake anamuuza zimenezi; ndipo mtima wake unamyuka m'kati mwake, iye nasanduka ngati mwala. 38Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa. 39#1Sam. 25.26, 34; 1Maf. 2.44; Mas. 7.16Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake. 40Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigaile ku Karimele, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wake. 41Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga. 42Ndipo Abigaile anafulumira nanyamuka, nakwera pa bulu, pamodzi ndi anamwali ake asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wake. 43Davide anatenganso Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo onse awiri anakhala akazi ake. 44#2Sam. 3.14Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu.
Currently Selected:
1 SAMUELE 25: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi