YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 14

14
Yonatani agonjetsa Afilisti
1Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake. 2Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi; 3#1Sam. 4.21ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka. 4Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene. 5Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba. 6#Ower. 7.2, 4, 7Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka. 7Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu. 8Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo. 9Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo. 10Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro. 11Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala. 12Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele. 13Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake. 14Kuwapha koyambako, Yonatani ndi wonyamula zida zake, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi. 15#2Maf. 7.7Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa. 16Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.
Saulo alumbirira anthu
17Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe. 18Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele. 19Ndipo kunali m'mene Saulo anali chilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'chigono cha Afilisti linachitikabe, nilikula; ndipo Saulo ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako. 20#Ower. 7.22Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu. 21Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m'dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani. 22#1Sam. 13.6Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko. 23#Eks. 14.30; Mas. 44.6-7Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni. 24Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya. 25#Eks. 3.8Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uchi pansi. 26Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo. 27Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. 28Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema. 29Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu. 30Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti. 31Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri. 32#Lev. 3.17Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi anaang'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wao. 33Pamenepo anauza Saulo, kuti, Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munachita konyenga; kunkhunizani mwala waukulu kwa ine lero. 34Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo. 35Ndipo Saulo anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.
Yonatani atsutsidwa afe
36Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno. 37Ndipo Saulo anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israele kodi? Koma Iye sanamyankhe tsiku lomweli. 38Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero. 39#2Sam. 12.5Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye. 40Ndipo iye ananena ndi Aisraele onse, Inu mukhale mbali ina, ndipo ine ndi Yonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, Chitani chimene chikukomerani. 41#Yos. 7.16-18Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka. 42Ndipo Saulo anati, Muchite maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Yonatani. 43#Yos. 7.19Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa. 44#1Sam. 14.39Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani.
Anthu alanditsa Yonatani
45 # 2Sam. 14.11; Mrk. 16.20; Luk. 21.18 Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi m'Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe. 46Ndipo Saulo analeka kuwapirikitsa Afilistiwo; ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.
47Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga. 48Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya.
49Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana akazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala; 50ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo. 51Ndipo atate wa Saulo ndiye Kisi; ndipo Nere atate wa Abinere ndiye mwana wa Abiyele.
52 # 1Sam. 8.11 Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.

Currently Selected:

1 SAMUELE 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in