YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 13

13
Nkhondo pakati pa Israele ndi Afilisti
1Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. 2Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao. 3Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. 4Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.
5Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni. 6Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje. 7Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.
Samuele adzudzula Saulo pa kupereka iye nsembe
8Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samuele; koma Samuele sanafike ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Saulo. 9Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo. 10Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye. 11Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi; 12chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumira, ndi kupereka nsembe yopsereza. 13#2Mbi. 16.9; 1Sam. 15.11Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha. 14#Mac. 13.22Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunga chimene Yehova anakulamulirani.
15Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi. 16Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi. 17Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala; 18gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.
19 # 2Maf. 24.14 Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo; 20koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake; 21ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu. 22Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo. 23Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi.

Currently Selected:

1 SAMUELE 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in