Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha. Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunga chimene Yehova anakulamulirani.