1 MAFUMU 3
3
Solomoni akwatira mwana wa Farao
1 #
1Maf. 6.1-38; 7.8; 9.24; 2Mbi. 8.11 Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu. 2#Deut. 12.2, 5Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo. 3#Deut. 6.5; 1Maf. 1.6, 14; Mas. 31.23; Aro. 8.28; 1Ako. 8.3Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.
Yehova aonekera Solomoni m'kulota usiku ku Gibiyoni
4 #
1Mbi. 21.29
Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi pa guwalo la nsembe. 5#Num. 12.6; Mat. 1.20Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse. 6#1Maf. 1.48; 2.4; Mas. 26.3Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino. 7#1Mbi. 29.1Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa. 8#Deut. 7.6Ndipo kapolo wanu ndili pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao. 9#2Mbi. 1.10; Mas. 72.1-2Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene? 10Ndipo mau amenewa anakondweretsa Yehova kuti Solomoni anapempha chimenechi. 11Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu; 12#1Maf. 4.29-31taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka. 13#Mat. 6.33; Aef. 3.20Ndiponso zimene sunazipempha adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse. 14#1Maf. 15.5Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako. 15Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.
Solomoni aweruza mlandu wa akazi awiri aja
16Pamenepo analowa kwa mfumu akazi awiri, ndiwo adama, naima pamaso pake. 17Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo. 18Ndipo kunachitika kuti tsiku lachitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo. 19Ndipo mwana wa mnzangayu anamwalira usiku, pokhala iyeyu anamgonera. 20Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m'tulo, namuika m'mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m'mfukato mwanga. 21Ndipo pouka ine m'mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona, ngwakufa, koma nditamzindikira m'mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai. 22Ndipo mkazi winayo anati, Iai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, Iai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu. 23Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, Iai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu. 24Niti mfumu, Kanditengereni chimpeni. Ndipo iwo anabwera ndi chimpeni kwa mfumu. 25Mfumu niti, Dula pakati mwana wamoyoyu, nupatse mmodzi chipinjiri, ndi wina chipinjiri chake. 26#Gen. 43.30; Yes. 49.15Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani. 27Pamenepo mfumu inayankha, niti, Mumpatse wachifundoyo mwana wamoyo, osamupha konse, uyo ndiye amake. 28#1Maf. 3.9, 11-12; 4.30-31Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.
Currently Selected:
1 MAFUMU 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi