1 MAFUMU 2
2
Davide atapangira Solomoni amwalira
1Pakuyandikira masiku ake a Davide akuti amwalire, analamulira Solomoni mwana wake, nati, 2#Yos. 1.7; 23.14Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu; 3#Deut. 29.9nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako; 4#Mas. 132.11-12kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele. 5#2Sam. 3.30, 39; 20.10Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake. 6Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere. 7#2Sam. 19.31-38Koma uchitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako. 8#2Sam. 16.5; 19.18, 23Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga. 9Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda. 10Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide. 11#1Mbi. 29.26-27Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu chitatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.
12Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.
Kulangidwa kwa Adoniya, Abiyatara, Yowabu ndi Simei
13 #
1Sam. 16.4-5
Pomwepo Adoniya mwana wa Hagiti anadza kwa Bateseba amai wake wa Solomoni, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene. 14Anatinso, Ndili nanu mau. Nati iye, Tanena. 15#1Mbi. 22.9-10Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova. 16Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena. 17#1Maf. 1.3-4Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomoni, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga. 18Ndipo Bateseba anati, Chabwino, ndidzakunenera kwa mfumu. 19#Eks. 20.12Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja. 20Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani. 21Ndipo iye anati, Abisagi wa ku Sunamu apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu akhale mkazi wake. 22Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya. 23Pomwepo mfumu Solomoni analumbira pa Yehova, nati, Mulungu andilange naonjezepo, zedi Adoniya wadziphetsa yekha ndi mau awa. 24#2Sam. 7.11-12Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wachifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe. 25Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye. 26#1Sam. 23.6Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo. 27#1Sam. 2.31-35Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli. 28#1Maf. 1.50Ndipo mbiriyi inamfika Yowabu, pakuti Yowabu anapatukira kwa Adoniya, angakhale sanapatukire kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anathawira ku chihema cha Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe. 29Ndipo anamuuza mfumu Solomoni, kuti, Yowabu wathawira ku chihema cha Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomoni anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwere. 30Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti. 31#Eks. 21.14; Ower. 9.24, 57; 1Maf. 2.5; Mas. 7.16Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa. 32Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pa mutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda. 33Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wake wa Yowabu, ndi pa mutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya. 34Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yakeyake kuchipululu. 35Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara. 36#1Maf. 2.8Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osatulukako kunka kwina konse. 37#2Sam. 15.23Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pa mutu wa iwe wekha. 38Ndipo Simei anena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzachita kapolo wanu. Ndipo Simei anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri. 39#1Sam. 27.2Ndipo kunachitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simei, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati. 40Ndipo Simei ananyamuka, namangirira mbereko pa bulu wake, namka ku Gati kwa Akisi kukafuna akapolo ake; namuka Simei, nabwera nao akapolo ake kuchokera ku Gati. 41Ndipo anamuuza Solomoni, kuti, Simei wachoka ku Yerusalemu kunka ku Gati, nabweranso. 42Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukuchenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakutuluka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino. 43Sunasunga chifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe? 44#2Sam. 16.5-13; Mas. 7.16Tsono mfumu inanenanso ndi Simei Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini. 45#Miy. 25.5Koma mfumu Solomoni adzadalitsika, ndi mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya. 46#2Mbi. 1.1Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.
Currently Selected:
1 MAFUMU 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi