YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 22

22
Ahabu apangana ndi Yehosafati
1Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo. 2#2Mbi. 18.2-34Koma kunachitika chaka chachitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israele. 3#Yos. 21.38Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu. 4#2Maf. 3.7Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako. 5Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero. 6Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu. 7#2Maf. 3.11Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye? 8Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu. 9Tsono mfumu ya Israele anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Imila. 10Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao. 11Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti. 12Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, ndipo mudzachita mwai; popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.
Mikaya anenera motsutsa Ahabu
13Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino. 14#Num. 22.38Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine. 15Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu. 16Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m'dzina la Yehova? 17#Mat. 9.36Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake. 18Pamenepo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuza kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa? 19#Yes. 6.1; Dan. 7.10; Mat. 18.10; Aheb. 1.7, 14Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere. 20Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti. 21Pamenepo mzimu wina unatuluka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani? 22#Ower. 9.23; 2Ate. 2.11Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene. 23#Ezk. 14.9Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena choipa cha inu. 24Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe? 25Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'chipinda cha pakati kubisala. 26Pamenepo inati mfumu ya Israele, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu; 27ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere. 28#Deut. 18.20-22Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Ahabu aphedwa mu nkhondo ya pa Aramu
29Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi. 30#2Mbi. 35.22Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo. 31Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha. 32Ndipo kunali, akapitao a magaleta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israele imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anafuula. 33Ndipo pamene akapitao a magaleta anaona kuti sindiye mfumu ya Israele, anabwerera osampirikitsa. 34Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa. 35Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'galeta mwake kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unatuluka m'bala pa phaka la galeta. 36Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumudzi kwao, ndi yense ku dziko la kwao. 37Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samariya, naika mfumu m'Samariya. 38#1Maf. 21.19Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo. 39Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 40Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ake; ndi Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Yehosafati mfumu ya Yuda
41Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele. 42Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu m'Yerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili. 43#1Maf. 15.14Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje. 44#2Mbi. 19.2; 2Ako. 6.14Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele. 45Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 46Ndipo anachotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wake Asa. 47#2Sam. 8.14Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu. 48#1Maf. 10.22; 2Mbi. 20.36-37Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere. 49Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana. 50Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Ahaziya mfumu Israele
51Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. 52#1Maf. 15.26Nachita choipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi ya amake, ndi ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene adachimwitsa Israele. 53#1Maf. 16.30-31Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele, monga umo anachitira atate wake.

Currently Selected:

1 MAFUMU 22: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in