1 MAFUMU 17
17
Mneneri Eliya ku Keriti
1 #
Luk. 4.25; Yak. 5.17 Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo. 2Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati, 3Choka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani. 4Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko. 5Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani. 6Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje. 7Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
Eliya aukitsa mwana wa wamasiye ku Zarefati
8Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati, 9#Luk. 4.26Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse. 10Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe. 11Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako. 12Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife. 13Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako. 14Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi. 15Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri. 16Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinachepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya. 17Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yake, analeka kupuma. 18#Luk. 4.34Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga? 19Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini. 20Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake? 21#2Maf. 4.34-35; Mac. 20.10Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m'chifuwa mwake. 22#Aheb. 11.35Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo. 23Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo. 24#Yoh. 3.2; 16.30Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
Currently Selected:
1 MAFUMU 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi