YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 1

1
Ukalamba wa Davide, atchula Solomoni wodzalowa m'malo mwake
1Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe. 2Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe. 3Tsono anafunafuna m'malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu. 4Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa. 5#2Sam. 15.1; 2Sam. 3.4Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga. 6Ndipo atate wake sadamvuta masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu. 7Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza. 8#2Sam. 23.8Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya. 9Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu; 10koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomoni mbale wake, sanawaitane. 11Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa? 12Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni. 13#1Maf. 1.30Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu? 14Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako. 15Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu. 16Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji? 17#1Maf. 1.13Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu. 18Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa. 19#1Maf. 1.25Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane. 20Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye. 21Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa. 22Ndipo taona, iye ali chilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo. 23Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. 24Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu? 25#1Sam. 10.24; 1Maf. 1.19Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya. 26Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane. 27Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye? 28Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bateseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu. 29Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse, 30#1Maf. 1.17zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe. 31#Neh. 2.3; Dan. 2.4Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya. 32Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu. 33Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni. 34#1Sam. 16.2, 13; 2Sam. 15.10Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. 35Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda. 36Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu. 37#Yos. 1.5, 17Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide. 38Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni. 39#Eks. 30.23-32; 1Sam. 10.24Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. 40Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang'ambika ndi phokoso lao. 41Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yowabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi chiyani kuti m'mudzi muli chibumo? 42#2Sam. 18.27Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino. 43Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomoni ufumu: 44ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu. 45Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo achokera kumeneko chikondwerere, ndi m'mudzimo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali. 46Ndiponso Solomoni wakhala pa chimpando cha ufumu. 47#1Maf. 1.37Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomoni lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wake wachifumu upose mpando wanu wachifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo. 48#Mas. 132.11-12Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere. 49Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anachita mantha, nanyamuka, napita yense njira yake. 50#1Maf. 2.28; Mas. 118.27Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe. 51Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga. 52#1Sam. 14.45; Mac. 27.34Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi. 53Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.

Currently Selected:

1 MAFUMU 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in