ZEKARIYA 14
14
Yehova adzathandiza a ku Yerusalemu polimbana ndi amitundu
1 #
Yes. 13.9
Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako. 2#Yow. 3.2Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mzindamo. 3Pamenepo Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana. 4#Ezk. 11.23; Yow. 3.12-14Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera. 5#Amo. 1.1; Mat. 24.30-31; 1Ate. 3.13Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu. 6Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada; 7#Yes. 60.19-20; Mat. 24.36koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbee. 8#Ezk. 47.1; Yoh. 4.10; Chiv. 22.1Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.
Yehova mfumu ya dziko lonse lapansi
9 #
Dan. 2.44; Aef. 4.5-6 Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha. 10Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu. 11#Yer. 23.5-6Ndipo anthu adzakhala m'menemo, ndipo sipadzakhalanso kuonongetsa; koma Yerusalemu adzakhala mosatekeseka. 12Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao. 13Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti chisokonezo chachikulu chochokera kwa Yehova chidzakhala pakati pao; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukira dzanja la mnzake. 14Ndi Yuda yemwe adzachita nkhondo ku Yerusalemu; ndi zolemera za amitundu onse ozungulirapo zidzasonkhanitsidwa, golide, ndi siliva, ndi zovala zambirimbiri. 15Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru, ngamira, ndi abulu, ndi nyama zonse zokhala m'misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo. 16#Yes. 60.6-7, 9Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa. 17Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula. 18Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa? 19Ili ndi tchimo la Ejipito, ndi tchimo la amitundu onse osakwerako kusunga chikondwerero cha Misasa. 20#Eks. 39.30; 1Ate. 3.13Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe. 21Inde mbiya zonse za mu Yerusalemu ndi mu Yuda zidzakhala zopatulikira Yehova wa makamu; ndi onse akuphera nsembe adzafika nadzatengako, ndi kuphikamo; ndipo tsiku lomwelo simudzakhalanso Mkanani m'nyumba ya Yehova wa makamu.
Currently Selected:
ZEKARIYA 14: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi