YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 13

13
Kuyeretsedwa kwa Yerusalemu
1 # Zek. 12.3-4, 6, 8, 11; Aheb. 9.14; 1Pet. 1.19; Chiv. 1.5 Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso. 2#Yos. 23.7; 2Pet. 2.1Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso. 3Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye. 4#Mik. 3.6-7Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzachita manyazi yense ndi masomphenya ake, ponenera iye; ndipo sadzavala chofunda chaubweya kunyenga nacho; 5koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga. 6Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.
7 # Yes. 40.11; Mat. 18.10, 14; 26.31; Mrk. 14.27; Yoh. 10.30; Afi. 2.6 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo. 8#Aro. 11.5Ndipo kudzachitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m'mwemo. 9#Mas. 50.15; Yes. 48.10; Hos. 2.23; 1Pet. 1.6-7Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.

Currently Selected:

ZEKARIYA 13: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for ZEKARIYA 13