1
1 YOHANE 4:18
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.
Compare
Explore 1 YOHANE 4:18
2
1 YOHANE 4:4
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi
Explore 1 YOHANE 4:4
3
1 YOHANE 4:19
Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.
Explore 1 YOHANE 4:19
4
1 YOHANE 4:7
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Explore 1 YOHANE 4:7
5
1 YOHANE 4:8
Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
Explore 1 YOHANE 4:8
6
1 YOHANE 4:10
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.
Explore 1 YOHANE 4:10
7
1 YOHANE 4:11
Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.
Explore 1 YOHANE 4:11
8
1 YOHANE 4:9
Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.
Explore 1 YOHANE 4:9
9
1 YOHANE 4:20
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.
Explore 1 YOHANE 4:20
10
1 YOHANE 4:15
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
Explore 1 YOHANE 4:15
11
1 YOHANE 4:21
Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.
Explore 1 YOHANE 4:21
12
1 YOHANE 4:1-2
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi. M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu
Explore 1 YOHANE 4:1-2
13
1 YOHANE 4:3
ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe
Explore 1 YOHANE 4:3
Home
Bible
Plans
Videos