Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.