Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza.