1
LUKA 6:38
Buku Lopatulika
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Compare
Explore LUKA 6:38
2
LUKA 6:45
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
Explore LUKA 6:45
3
LUKA 6:35
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
Explore LUKA 6:35
4
LUKA 6:36
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
Explore LUKA 6:36
5
LUKA 6:37
Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.
Explore LUKA 6:37
6
LUKA 6:27-28
Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.
Explore LUKA 6:27-28
7
LUKA 6:31
Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.
Explore LUKA 6:31
8
LUKA 6:29-30
Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako. Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.
Explore LUKA 6:29-30
9
LUKA 6:43
Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino.
Explore LUKA 6:43
10
LUKA 6:44
Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa.
Explore LUKA 6:44
Home
Bible
Plans
Videos