chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita. Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.