Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.