YOHANE 12

12
Maria adzoza mapazi a Yesu
(Mat. 26.6-13; Mrk. 14.3-9)
1 # Yoh. 11.1, 43 Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa. 2#Yoh. 11.2Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye. 3#Yoh. 11.2Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo. 4Koma Yudasi Iskariote, mmodzi wa ophunzira ake, amene adzampereka Iye, ananena, 5Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwe chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka? 6#Yoh. 13.29Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo. 7Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga. 8#Mat. 26.11Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.
9 # Yoh. 11.43-44 Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa. 10Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso; 11#Yoh. 11.45pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.
Yesu alowa mu Yerusalemu
(Mat. 21.1-12; Mrk. 11.1-10; Luk. 19.28-40)
12 # Mat. 21.8 M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu, 13#Mas. 118.26anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele. 14#Mat. 21.7Koma Yesu, m'mene adapeza kabulu anakhala pamenepo; monga mulembedwa: 15#Zek. 9.9Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu. 16#Luk. 18.34; Yoh. 2.22; 14.26Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi. 17Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni. 18Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi. 19#Yoh. 11.47-48Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.
Agriki afuna kuona Yesu; Iye ayankhapo
20 # 1Maf. 8.41-43; Mac. 17.4 Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero. 21#Yoh. 1.44Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu. 22Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu. 23#Yoh. 17.1Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. 24#1Ako. 15.36Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri. 25#Mat. 10.39Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha. 26#Yoh. 17.24Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu. 27#Mat. 26.38-39Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi. 28#Mat. 10.40Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso. 29Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye. 30#Yoh. 11.42Yesu anayankha nati, Mau awa sanafike chifukwa cha Ine, koma cha inu. 31Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano. 32#Yoh. 3.14Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha. 33Koma ananena ichi ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo. 34#Mas. 89.35-37; Ezk. 37.24-25Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani? 35#Yer. 13.16; Yoh. 11.10; Aef. 5.8Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako. 36#Yer. 13.16; Yoh. 11.10; Aef. 5.8Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira. 37Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye; 38#Yes. 53.1; Aro. 10.16kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,
Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?
Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?
39Chifukwa cha ichi sanathe kukhulupirira, pakuti Yesaya anatinso,
40 # Yes. 6.9-10 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;
kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,
nangatembenuke,
ndipo ndingawachiritse.
41 # Yes. 6.1 Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake; nalankhula za Iye. 42#Yoh. 7.13; 9.22Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge, 43#Yoh. 5.44pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.
44 # Mat. 10.40 Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine. 45#Yoh. 10.30Ndipo wondiona Ine aona amene anandituma Ine. 46#Yoh. 1.9Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima. 47#Yoh. 3.17Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadze kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi. 48#Yoh. 3.18; Deut. 18.18-19Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza. 49#Deut. 18.18-19Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. 50Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula.

المحددات الحالية:

YOHANE 12: BLP-2018

تمييز النص

شارك

نسخ

None

هل تريد حفظ أبرز أعمالك على جميع أجهزتك؟ قم بالتسجيل أو تسجيل الدخول