YOHANE 11

11
Chiukitso cha Lazaro
1 # Luk. 10.38-39 Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita. 2#Yoh. 12.2Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala. 3Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala. 4#Yoh. 9.3Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako. 5Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro. 6#Yoh. 10.40Chifukwa chake pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pamalo pomwepo masiku awiri. 7Ndipo pambuyo pake ananena kwa ophunzira ake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya. 8#Yoh. 10.31Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi? 9Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi. 10#Yoh. 12.35Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye. 11#Deut. 31.16; Mat. 9.24; Mac. 7.60; 1Ako. 15.18, 51Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. 12Chifukwa chake ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzachira. 13Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo. 14Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. 15Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye. 16Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.
17Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai. 18Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; 19koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao. 20Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi Iye; koma Maria anakhalabe m'nyumba. 21Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. 22Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. 23Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. 24#Luk. 14.14Marita ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomaliza. 25#Yoh. 6.39-40, 44Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; 26#Yoh. 6.39-40, 44ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi? 27#Mat. 16.16; Yoh. 6.69Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi. 28Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe. 29Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa Iye. 30(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye.) 31Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko. 32#Yoh. 11.21Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. 33Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, 34nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone. 35#Luk. 19.41Yesu analira. 36Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi! 37#Yoh. 9.6Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sakanatha kodi kuchita kuti asafe ameneyunso? 38Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo. 39Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai. 40#Yoh. 11.4, 23Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu? 41Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine. 42#Yoh. 12.30Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 43Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka. 44#Yoh. 20.7Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
45 # Yoh. 10.42 Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye. 46Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazichita.
Afarisi apangana za kupha Yesu
(Mat. 26.1-5; Mrk. 14.1-2; Luk. 22.1-2)
47 # Mas. 2.2; Mat. 26.3 Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. 48Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu. 49#Yoh. 18.14Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu, 50#Yoh. 18.14kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke. 51Koma ichi sananene kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu adzafera mtunduwo; 52ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo. 53Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye.
54 # Yoh. 7.1 Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake. 55Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha. 56#Yoh. 7.11Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzake poimirira iwo mu Kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuchikondwerero kodi? 57Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.

المحددات الحالية:

YOHANE 11: BLP-2018

تمييز النص

شارك

نسخ

None

هل تريد حفظ أبرز أعمالك على جميع أجهزتك؟ قم بالتسجيل أو تسجيل الدخول