LUKA 18

18
Fanizo la woweruza wosalungama
1 # Aro. 12.12; Aef. 6.18 Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima; 2nanena, M'mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. 3Ndipo m'mzinda momwemo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane. 4Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu; 5#Luk. 11.8koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake. 6Ndipo Ambuye anati, Tamverani chonena woweruza wosalungama. 7#Chiv. 6.10Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima? 8Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?
Fanizo la Mfarisi ndi wamsonkho
9 # Luk. 10.29 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili, 10Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. 11#Chiv. 3.17Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; 12ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo. 13Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa. 14#Mat. 23.12Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.
Yesu adalitsa ana
(Mat. 19.13-15; Mrk. 10.13-16)
15Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. 16#1Ako. 14.20Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. 17Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.
Mkulu mwini chuma
(Mat. 19.16-30; Mrk. 10.17-31)
18Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha? 19Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu. 20#Eks. 20.12-16; Aro. 13.9; Aef. 6.2Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako. 21Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga. 22#Mat. 6.19-20; 1Tim. 6.19Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. 23Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri. 24#Mrk. 10.23Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! 25Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali. 26Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa? 27#Yer. 32.17Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu. 28Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu. 29Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum'bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, 30koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi ino; ndipo m'nthawi ilinkudza moyo wosatha.
Yesu aneneratu za mazunzo ake
(Mat. 20.17-19; Mrk. 10.32-34)
31 # Mas. 22; Yes. 53 Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri. 32#Mat. 27.2, 27-31Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu; 33ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka. 34#Mrk. 9Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo.
Msaona wa ku Yeriko
(Mat. 20.29-34; Mrk. 10.46-52)
35Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha; 36ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, Ichi nchiyani? 37Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita. 38Ndipo anafuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. 39Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. 40Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye, 41Ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso. 42#Luk. 17.19Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. 43#Mac. 4.21Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.

Okuqokiwe okwamanje:

LUKA 18: BLP-2018

Qhakambisa

Dlulisela

Kopisha

None

Ufuna ukuthi okuvelele kwakho kugcinwe kuwo wonke amadivayisi akho? Bhalisa noma ngena ngemvume