Gen. 5
5
Mibadwo yochokera mwa Adamu
(1 Mbi. 1.1-4)
1 #
Gen. 1.27, 28 Mndandanda wa mibadwo yochokera mwa Adamu udayenda motere: (Mulungu polenga Adamu, adampanga muchifaniziro chake. 2#Mt. 19.4; Mk. 10.6 Adalenga mwamuna ndi mkazi, ndipo adaŵadalitsa, naŵatchula dzina loti Anthu.) 3Adamu ali wa zaka 130 adabereka mwana wofanafana ndi iye, namutcha Seti. 4Pambuyo pake Adamu adakhala ndi moyo zaka zinanso 800. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 5Adamwalira ali wa zaka 930.
6Seti ali wa zaka 105, adabereka mwana dzina lake Enosi, 7ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 807. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 8Adamwalira ali wa zaka 912. 9Enosi ali wa zaka 90, adabereka mwana dzina lake Kenani, 10ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 815. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11Adamwalira ali wa zaka 905.
12Kenani ali wa zaka 70, adabereka mwana dzina lake Mahalalele, 13ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 840. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14Adamwalira ali wa zaka 910.
15Mahalalele ali wa zaka 65 adabereka Yaredi, 16ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 830. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17Adamwalira ali wa zaka 895.
18Yaredi ali wa zaka 162, adabereka mwana dzina lake Enoki, 19ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 800. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20Adamwalira ali wa zaka 962.
21Enoki ali wa zaka 65, adabereka mwana dzina lake Metusela. 22Enoki adakhala ndi moyo zaka zina 300, akuyanjana ndi Mulungu. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23Adamwalira ali wa zaka 365. 24#Mphu. 44.16; 49.14; Ahe. 11.5; Yuda 1.14Iyeyu adayanjana ndi Mulungu moyo wake wonse. Ndipo sadaonekenso, chifukwa choti Mulungu adamtenga.
25Metusela ali wa zaka 187, adabereka mwana dzina lake Lameki, 26ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 782. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27Adamwalira ali wa zaka 969. 28Lameki ali wa zaka 182, adabereka mwana, 29ndipo adati, “Mwana ameneyu adzatipumuza ku ntchito zathu zolemetsazi zolima nthaka imene Chauta adaitemberera.” Ndipo mwanayo adamutcha dzina lake Nowa. 30Lameki adakhalanso ndi moyo zaka zina 595. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31Adamwalira ali wa zaka 777.
32Nowa ali wa zaka zopitirira 500, adabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.
Bible Society of Malawi