1
Yohane 10:10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
Karşılaştır
Yohane 10:10 keşfedin
2
Yohane 10:11
“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Yohane 10:11 keşfedin
3
Yohane 10:27
Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.
Yohane 10:27 keşfedin
4
Yohane 10:28
Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.
Yohane 10:28 keşfedin
5
Yohane 10:9
Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.
Yohane 10:9 keşfedin
6
Yohane 10:14
“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa
Yohane 10:14 keşfedin
7
Yohane 10:29-30
Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. Ine ndi Atate ndife amodzi.”
Yohane 10:29-30 keşfedin
8
Yohane 10:15
monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Yohane 10:15 keşfedin
9
Yohane 10:18
Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
Yohane 10:18 keşfedin
10
Yohane 10:7
Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
Yohane 10:7 keşfedin
11
Yohane 10:12
Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.
Yohane 10:12 keşfedin
12
Yohane 10:1
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.
Yohane 10:1 keşfedin
Ana Sayfa
Kutsal Kitap
Okuma Planları
Videolar