Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Lk. 7

7
Za mkulu wa asilikali wachiroma
(Mt. 8.5-13; Yoh. 4.43-54)
1Yesu atatsiriza kulankhula zonsezi ndi anthu aja, adapita ku Kapernao. 2Tsono mkulu wina wa gulu la asilikali achiroma 100 anali ndi wantchito amene ankamukonda kwambiri. Wantchitoyo ankadwala, ndipo anali pafupi kufa. 3Mkuluyo atamva za Yesu, adatuma akulu ena a Ayuda kwa Iye kukampempha kuti adzachiritse wantchito wakeyo. 4Pamene adafika kwa Yesu, adampempha kolimba namuuza kuti, “Ameneyu ngwoyeneradi kuti mumchitire zimenezi, 5chifukwa amaukonda mtundu wathu, mwakuti adatimangira nyumba yamapemphero.”
6Tsono Yesu adapita nawo. Pamene Iye ankayandikira nyumba yake, mkulu wa asilikali uja adatuma abwenzi ake kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, musadzivute, pakuti sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. 7Nchifukwa chake sindidadziyesenso woyenera kudza kwa Inu. Koma mungonena mau okha kuti wantchito wanga achire. 8Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita’, amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera’, amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti’, amachitadi.”
9Yesu atamva zimenezi, adachita naye chidwi. Adatembenuka nauza chinamtindi cha anthu amene ankamutsata aja kuti, “Ndithudi, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.” 10Otumidwa aja adabwerera kunyumba, nakapeza wantchito uja atachiritsidwa.
Yesu aukitsa mwana wa mai wamasiye wa ku Naini
11Pambuyo pake Yesu adapita ku mudzi wina, dzina lake Naini. Ophunzira ake pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri adatsagana naye. 12Pamene Yesu ankayandikira chipata cha mudziwo, adakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna. Mai wake wa mwanayo anali wamasiye, ndipo mwana wake anali yekhayo. Anthu ambirimbiri am'mudzimo anali naye. 13Pamene Ambuye adamuwona, adamumvera chisoni, namuuza kuti, “Mai, musalire.” 14Tsono adafika pafupi nakhudza chithathacho. Anthu amene ankanyamula malirowo adaima, ndipo Yesu adati, “Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka.” 15Pamenepo wakufayo adakhala tsonga nayamba kulankhula, Yesu nkumupereka kwa mai wake. 16Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.” 17Mbiri ya Yesuyi idawanda m'dziko lonse la Yudeya, ndi ku madera onse ozungulira.
Yohane Mbatizi atuma amithenga kwa Yesu
(Mt. 11.2-19)
18Ophunzira a Yohane adamsimbira zonsezi Yohaneyo. 19Tsono iye adaitanapo ophunzira ake ena aŵiri, naŵatuma kwa Ambuye kukaŵafunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” 20Pamene iwo adafika kwa Yesu, adamuuza kuti, “Yohane Mbatizi watituma kwa Inu kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Inuyo ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?’ ” 21Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri. 22#Yes. 35.5, 6; Yes. 61.1Tsono Iye adayankha ophunzira a Yohane aja kuti, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mwaona ndi kuzimva. Akhungu akupenya, opunduka miyendo akuyenda, akhate akuchira, agonthi akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino. 23Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
24Amithenga a Yohane aja atachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 25Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zakaso ndi okonda madyerero amakhala m'nyumba za mafumu. 26Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri. 27#Mal. 3.1Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti,
“ ‘Nayitu nthumwi yanga,
ndikuituma m'tsogolo mwako,
kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’
28“Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wa Mulungu amampambana. 29#Mt. 21.32; Lk. 3.12Anthu onse, ndi okhometsa msonkho omwe, adamva mau a Yohane, ndipo pakubatizidwa ndi Yohaneyo adavomereza kuti Mulungu ngwolungama. 30Koma Afarisi ndi akatswiri a Malamulo, pakukana kubatizidwa ndi iye, adakana okha zimene Mulungu adafuna kuŵachitira.
31“Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati chiyani? 32Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti,
“ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati,
bwanji inu osavina?
Tidaabuma maliro,
bwanji inu osalira?’
33“Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndipo sankamwa vinyo, inu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mizimu yoipa.’ 34Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ 35Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”
Mai wochimwa adzoza mapazi a Yesu
36Wina wa m'gulu la Afarisi adaitana Yesu kuti akadye kwao. Yesu adapita nakaloŵa m'nyumba ya Mfarisiyo nkukakhala podyera. 37#Mt. 26.7; Mk. 14.3; Yoh. 12.3M'mudzimo mudaali mai wachiwerewere. Iyeyu atamva kuti Yesu akudya m'nyumba ya Mfarisi uja, adabwera ndi nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira. 38Adakagwada kumbuyo, ku mapazi a Yesu, akulira, nayamba kukhetsera misozi pa mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi la kumutu kwake. Adampsompsonanso mapazi akewo, naŵadzoza ndi mafuta aja.
39Koma Mfarisi amene adaaitana Yesu uja ataona zimenezi, adayamba kuganiza kuti, “Munthuyu akadakhaladi mneneri, bwenzi atamdziŵa mai amene akumkhudzayu, kuti ndi wachiwerewere.” 40Apo Yesu adamuuza kuti, “Simoni, ndili ndi nkhani yoti ndikuuze.” Iye adati, “Aphunzitsi, nenani.” 41Yesu adati, “Panali anthu aŵiri amene adaakongola ndalama kwa munthu wokongoza ndalama. Wina adaakongola ndalama makumi asanu, wina ndalama zisanu. 42Popeza kuti adaalibe choti abwezere, adaŵakhululukira ngongolezo onse aŵiri. Tsono iweyo ukuganiza kuti mwa aŵiriŵa ndani adzakonde wokongozayo koposa?” 43Simoni adati, “Ndiyesa koma amene adamkhululukira zambiri uja.” Yesu adamuuza kuti, “Wayankha bwino.”
44Atatero, Yesu adacheukira mai uja, nauza Simoni kuti, “Ukumuwona maiyu? Ine ndaloŵa m'nyumba mwako muno, iwe sudandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma iyeyu wakhala akukhetsera misozi pa mapazi anga, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. 45Iwe sudandimpsomphsone, koma iyeyu chiloŵere changa muno, wakhalira kumpsompsona mapazi anga osalekeza. 46Iwe sudandidzoze kumutu kwanga ndi mafuta, koma iyeyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira. 47Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”
48Ndipo Yesu adauza mai uja kuti, “Machimo ako akhululukidwa.” 49Apo amene ankadya naye adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Kodi ndani uyu wokhululukira ndi machimo omweyu?” 50Koma Yesu adauza maiyo kuti, “Chikhulupiriro chanu chakupulumutsani. Pitani ndi mtendere.”

Kasalukuyang Napili:

Lk. 7: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in