Gen. 39
39
Yosefe ndi mkazi wa Potifara
1Aismaele aja adapita naye Yosefe ku Ejipito kumene Potifara Mwejipito, nduna ya Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda kunyumba ya mfumu, adamgula. 2#Ntc. 7.9 Chauta anali naye Yosefe, ndipo adamthandiza kuti zonse zimuyendere bwino. Adakhala m'nyumba ya bwana wake, Mwejipito uja. 3Bwana wakeyo adaona kuti Chauta anali naye Yosefe, ndi kuti ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita. 4Potifara adakondwa naye Yosefe poona m'mene ankamutumikira. Choncho adamsandutsa kapitao wa nyumba yake, ndiponso woyang'anira zonse zam'nyumbamo. 5Kuyambira nthaŵi imene Yosefe adayamba kusamalira zonse za m'nyumba ya Potifarayo, Chauta adadalitsa zonse za kunyumba kwa Mwejipitoyo, ngakhale za kuminda kwake, chifukwa cha Yosefeyo. 6Choncho Potifara adaika m'manja mwa Yosefe zake zonse, kotero kuti sankalabadiranso kanthu kalikonse, koma chakudya chokha chimene ankadya.
Yosefe anali wa maonekedwe abwino ndi wokongola. 7Patapita kanthaŵi, mkazi wa bwana wake adayamba kusirira Yosefe. Tsono mkaziyo adauza Yosefeyo kuti, “Bwanji ugone nane.” 8Yosefe adakana, adati, “Chifukwa choti ine ndikugwira ntchito muno, bwana wanga salabadiranso kanthu kalikonse ka m'nyumba muno. Adandipatsa ukapitao woyang'anira zake zonse, 9ndipo ulamuliro wa zonse za m'nyumba muno uli m'manja mwanga, osati m'manja mwake. Sadandimane kanthu kalikonse kupatula inu nokha, pakuti ndinu mkazi wake. Tsono kungatheke bwanji kuti ine ndichite chinthu choipitsitsa choterechi, ndi kuchimwira Mulungu?” 10Ngakhale mkazi uja ankalankhula mau ameneŵa kwa Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefeyo sankamvako mpang'ono pomwe, ndipo sankalola kuchita naye zoipa. 11Koma tsiku lina Yosefe adaloŵa m'nyumba kuti agwire ntchito, ndipo panalibe antchito ena m'nyumbamo. 12Mkazi uja adamgwira mwinjiro Yosefeyo, namuuza kuti, “Ugone nane basi!” Koma iye adathaŵira pabwalo, kusiya mwinjiro uja uli m'manja mwa mkaziyo. 13Tsono mkazi uja ataona kuti Yosefe wasiya mwinjiro ndipo wathaŵira pabwalo, 14adaitana antchito am'nyumbamo, naŵauza kuti, “Mwaziwona izi? Mwamuna wanga adabwera ndi Muhebri uyu m'nyumba muno kudzatipunza ife. Iye anakaloŵa kuchipinda kwanga nandinyenga kuti ndigone naye. Koma ine ndinakuŵa kwambiri. 15Tsono atamva kukuwa kwangako, wasiya mwinjiro wake m'manja mwangamu nkuthaŵira pabwalo.” 16Mwinjirowo adangousunga m'manja kudikira mpaka bwana wa Yosefe atabwera. 17Tsono atabwera, adamsimbira nkhani yonseyo, adati, “Kapolo uja Wachihebri mudabwera naye m'nyumba munoyu, analoŵa kuchipinda kwanga kukandipunza ine. 18Koma ine nditakuwa, iyeyo anasiya mwinjiro wake pafupi ndi ine, nkuthaŵira pabwalo.”
19Mbuyake wa Yosefe adapsa mtima koopsa atamva mau a mkazi wake onena kuti, “Inde, izi ndi zimene wandichita kapolo wanu.” 20Pompo adammangitsa Yosefe nakamtsekera m'ndende m'mene ankasungamo akaidi a mfumu, ndipo adakhala m'menemo. 21#Ntc. 7.9 Koma Chauta anali naye Yosefe, namkomera mtima kwambiri, kotero kuti wosunga ndende adakondwera naye Yosefe. 22Adamsandutsa kapitao woyang'anira akaidi anzake onse, pamodzi ndi zonse zochitika m'ndendemo. 23Zonse zinali m'manja mwa Yosefe, ndipo wosunga ndendeyo sankayang'aniranso kanthu kena kalikonse, chifukwa Chauta anali naye Yosefe ndipo ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita.
ที่ได้เลือกล่าสุด:
Gen. 39: BLY-DC
เน้นข้อความ
แบ่งปัน
คัดลอก

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้
Bible Society of Malawi