Gen. 39:7-9
Gen. 39:7-9 BLY-DC
Patapita kanthaŵi, mkazi wa bwana wake adayamba kusirira Yosefe. Tsono mkaziyo adauza Yosefeyo kuti, “Bwanji ugone nane.” Yosefe adakana, adati, “Chifukwa choti ine ndikugwira ntchito muno, bwana wanga salabadiranso kanthu kalikonse ka m'nyumba muno. Adandipatsa ukapitao woyang'anira zake zonse, ndipo ulamuliro wa zonse za m'nyumba muno uli m'manja mwanga, osati m'manja mwake. Sadandimane kanthu kalikonse kupatula inu nokha, pakuti ndinu mkazi wake. Tsono kungatheke bwanji kuti ine ndichite chinthu choipitsitsa choterechi, ndi kuchimwira Mulungu?”