Gen. 35

35
Mulungu adalitsa Yakobe ku Betele
1 # Gen. 28.11-17 Tsono Mulungu adauza Yakobe kuti, “Nyamuka, pita ku Betele, ukakhale komweko. Ukamangeko guwa la Mulungu amene adakuwonekera pamene unkathaŵa mbale wako Esau.” 2Motero Yakobe adauza banja lake ndi onse amene anali naye kuti, “Tayani milungu yachilendo imene muli nayo pakati panu. Mudziyeretse, ndipo muvale zovala zaudongo. 3Tichokako kuno, tipita ku Betele kumene ndikamange guwa la Mulungu amene adandithandiza pa nthaŵi ya mavuto anga. Ndiye ndithu amene wakhala nane kulikonse komwe ndinkapita.” 4Motero milungu yonse yachilendo imene ana ake anali nayo, adaipereka kwa Yakobe, pamodzinso ndi ndolo zakukhutu zimene ankavala. Zonsezo adazifotsera patsinde pa mtengo wa thundu pafupi ndi Sekemu.
5Pamene Yakobe ndi ana ake adachoka, anthu onse a mizinda yozungulira adachita mantha, motero sadaŵatsatire. 6Tsono Yakobe adafika ndi anthu ake ku Luzi (ndiye kuti Betele) m'dziko la Kanani. 7Adamanga guwa kumeneko, ndipo malowo adaŵatcha Betele, chifukwa kumeneko nkumene Mulungu adadziwulula kwa Yakobe pamene ankathaŵa mbale wake. 8Debora mlezi wa Rakele, adamwalira komweko, ndipo adaikidwa patsinde pa mtengo wathundu ku Beteleko. Motero malowo adatchedwa Mtengo Wamaliro.
9Yakobe atabwerako ku Mesopotamiya kuja, Mulungu adamuwonekeranso namudalitsa. 10#Gen. 32.28 Mulungu adati, “Dzina lako ndiwe Yakobe, koma kuyambira tsopano, dzina lako lidzakhala Israele.” Motero adayamba kutchedwa Israele. 11#Gen. 17.4-8 Pambuyo pake Mulungu adamuuza kuti, “Ine ndine Mulungu, Mphambe. Ubale ana ambiri. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Zidzukulu zako zidzachuluka kwambiri, kotero kuti zidzakhala mitundu yambiri ya anthu. 12Ndidzakupatsa dziko limene ndidapatsa Abrahamu ndi Isaki. Dziko limeneli ndidzapatsanso zidzukulu zako, iwe utafa.” 13Tsono Mulungu adamsiya Yakobe pa malo omwe ankalankhula nayepo, napita. 14#Gen. 28.18, 19 Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa malo amenewo. Adapereka chopereka cha chakumwa pamwalapo, nathirapo mafuta. 15Malo amene Mulungu adalankhula naye, Yakobe adaŵatcha Betele.
Imfa ya Rakele
16Tsono onse adachoka ku Betele, koma asanafike ku Efurata, nthaŵi yoti Rakele aone mwana idamukwanira, ndipo kubereka kwake kudamuvuta kwambiri. 17Zidafika poipa kwambiri, ndipo mzamba adamuuza kuti, “Musaope, ameneyu ndi mwana wina wamwamuna.” 18Tsono Rakele akumwalira kumene, akupuma mwaŵefuŵefu, kutsirizika, adamutcha mwanayo Benoni, koma bambo wake adamutcha Benjamini. 19Rakele atamwalira, adaikidwa pambali pa mseu wopita ku Efurata (ndiye kuti Betelehemu.) 20Ndipo Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa manda a Rakele. Mwalawo ulipobe pamenepo mpaka lero lino. 21Yakobe adapitirira nakamanga mahema ake kuseri kwa nsanja ya Edere.
Ana a Yakobe
(1 Mbi. 2.1-2)
22 # Gen. 49.4 Pamene Yakobe ankakhala m'dziko limenelo, Rubeni adaachita zoipa ndi Biliha, mmodzi wa azikazi a bambo wake, Yakobeyo nkuzimva zimenezo. Yakobe anali ndi ana aamuna khumi ndi aŵiri.
23Ana a Leya anali aŵa: Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni. 24Ana a Rakele anali aŵa: Yosefe ndi Benjamini. 25Ana a Biliha mdzakazi wa Rakele anali aŵa: Dani ndi Nafutali. 26Ana a Zilipa mdzakazi wa Leya anali aŵa: Gadi ndi Asere. Ameneŵa ndiwo ana a Yakobe amene adabadwira ku Mesopotamiya.
Imfa ya Isaki
27 # Gen. 13.18 Yakobe adakafika kwa bambo wake Isaki ku Mamure (kumenenso kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapena Hebroni), kumene Abrahamu ndi Isaki ankakhala kale. 28Tsono Isaki adamwalira ali wa zaka 180. 29Ndipo adafa ndi kuikidwa m'manda, ali nkhalamba zedi. Ana ake, Esau ndi a Yakobe ndiwo adamuika m'manda.

ที่ได้เลือกล่าสุด:

Gen. 35: BLY-DC

เน้นข้อความ

แบ่งปัน

คัดลอก

None

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้

วิดีโอสำหรับ Gen. 35