Pomwepo Yakobe adalumbira kwa Mulungu, adati, “Mukakhala nane ndi kunditchinjiriza pa ulendo wangawu, ndipo mukandipatsa chakudya ndi zovala, ndi kundibwezera bwino kwathu kwa atate anga, mudzakhala Mulungu wanga. Mwala wachikumbutso ndauimiritsawu udzakhala nyumba yanu, ndipo ine ndidzakupatsani gawo lachikhumi la zonse zimene mudzandipatse.”