GENESIS 29

29
Yakobo akomana ndi Rakele
1Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa. 2Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu. 3Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake. 4Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani. 5Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa. 6Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa. 7Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni. 8Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa. 9#Eks. 2.16-17Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta. 10Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake. 11Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ake, nalira. 12Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake.
Labani alandira Yakobo
13 # Gen. 24.28-29 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo. 14Ndipo Labani anati kwa iye, Etu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi. 15Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani? 16Ndipo Labani anali ndi ana akazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele. 17Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola. 18Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono. 19Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine. 20#Gen. 30.26; Hos. 12.12Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.
Leya ndi Rakele
21Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye. 22Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero. 23Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wake wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo. 24Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya. 25Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji? 26Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkulu. 27Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri. 28Yakobo ndipo anachita chotero namaliza sabata lake; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wake wamkazi kuti akwatire iyenso. 29Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Rakele. 30Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.
Ana a Yakobo
31 # Deut. 21.15 Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma. 32Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine. 33Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni. 34Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi. 35#Gen. 49.8Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.

தற்சமயம் தேர்ந்தெடுக்கப்பட்டது:

GENESIS 29: BLPB2014

சிறப்புக்கூறு

பகிர்

நகல்

None

உங்கள் எல்லா சாதனங்களிலும் உங்கள் சிறப்பம்சங்கள் சேமிக்கப்பட வேண்டுமா? பதிவு செய்யவும் அல்லது உள்நுழையவும்