LUKA 17
17
Za zolakwitsa, ndi makhululukidwe, ndi mphamvu ya chikhulupiriro ndi kutumikira kwathu
(Mat. 18.6-7, 21-22; Mrk. 9.42)
1 #
Mat. 18.6-7; 1Ako. 11.19 Ndipo anati kwa ophunzira ake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo. 2Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali. 3#Mat. 18.15, 21Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire. 4Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.
5Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro. 6#Mat. 17.20Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu. 7Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya; 8wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe? 9Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa? 10#1Ako. 9.16-17Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.
Yesu achiritsa akhate khumi
11Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu Iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya. 12#Lev. 13.46Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali; 13ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo. 14#Mat. 8.4Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa. 15Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau aakulu; 16ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo. 17Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja? 18Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeke mmodzi kodi, koma mlendo uyu? 19#Mat. 9.22Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.
Za kufikanso kwa Ambuye
(Mat. 24.23-28, 37-41)
20Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe; 21#Aro. 14.17ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.
22 #
Mat. 9.15
Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. 23#Mat. 24.23Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! Taonani ili? Musachoka kapena kuwatsata; 24#Mat. 24.27pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake. 25#Mrk. 8.31Koma ayenera ayambe wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno. 26#Gen. 7Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu. 27Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo. 28#Gen. 19Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; 29koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu udavumba moto ndi sulufure zochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo; 30momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu. 31#Mat. 24.17-18; Mrk. 13.15-16Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa tsindwi, ndi akatundu ake m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zake za m'mbuyo. 32#Gen. 19.26Kumbukirani mkazi wa Loti. 33#Mat. 10.39; Mrk. 8.35Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga. 34#Mat. 24.40-41; 1Ate. 4.17Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. 35#Mat. 24.40-41; 1Ate. 4.17Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.#17.35 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 36 Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. 37#Mat. 24.28Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.
தற்சமயம் தேர்ந்தெடுக்கப்பட்டது:
LUKA 17: BLP-2018
சிறப்புக்கூறு
பகிர்
நகல்
உங்கள் எல்லா சாதனங்களிலும் உங்கள் சிறப்பம்சங்கள் சேமிக்கப்பட வேண்டுமா? பதிவு செய்யவும் அல்லது உள்நுழையவும்
Bible Society of Malawi