1
Marko 14:36
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
ஒப்பீடு
Marko 14:36 ஆராயுங்கள்
2
Marko 14:38
Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”
Marko 14:38 ஆராயுங்கள்
3
Marko 14:9
Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
Marko 14:9 ஆராயுங்கள்
4
Marko 14:34
Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”
Marko 14:34 ஆராயுங்கள்
5
Marko 14:22
Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
Marko 14:22 ஆராயுங்கள்
6
Marko 14:23-24
Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo. Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri.
Marko 14:23-24 ஆராயுங்கள்
7
Marko 14:27
Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha Mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’
Marko 14:27 ஆராயுங்கள்
8
Marko 14:42
Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”
Marko 14:42 ஆராயுங்கள்
9
Marko 14:30
Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”
Marko 14:30 ஆராயுங்கள்
முகப்பு
வேதாகமம்
வாசிப்புத் திட்டங்கள்
காணொளிகள்