Gen. 20
20
Abrahamu ndi Abimeleki
1Abrahamu adachokako ku Mamure kuja napita ku Negebu, chigawo chakumwera. Adakakhala pakati pa mzinda wa Kadesi ndi dziko la Suri, nakhazikika ku dziko la Gerari. 2#Gen. 12.13; 26.7 Kumeneko adauza anthu kuti, “Sarayu ndi mlongo wanga.” Motero Abimeleki, mfumu ya ku Gerari, adamtenga Sarayo. 3Tsono Mulungu adamuwonekera usiku m'maloto nati, “Ufatu iwe chifukwa mkazi watengayu ndi wokwatiwa.” 4Koma Abimeleki anali asanamkhudze mkaziyo, choncho adati, “Ambuye, kodi Inu mungaphedi munthu wosalakwa? 5Abrahamu pondiwuza adati, ‘Ndi mlongo wanga,’ ndipo iyenso mwini wake ankanena kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Ine pochita zimenezi, mtima wanga sudanditsutse konse, ndipo sindidalakwe.” 6Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo. 7Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.”
8M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abimeleki adaitana antchito ake onse naŵauza zonsezi, ndipo anthuwo adachita mantha kwambiri. 9Tsono Abimeleki adaitana Abrahamu namufunsa kuti, “Kodi iwe watichita zotani? Kodi ine ndakulakwira chiyani, kuti iweyo undiputire chilango chotere ine ndi onse a mu ufumu wanga? Zimene wandichitazi nzosayenera konse kuzichita. 10Chifukwa chiyani wachita zimenezi?” 11Abrahamu adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibe ndi mmodzi yemwe woopa Mulungu, ndipo kuti akadandipha nkutenga mkazi wangayu. 12Komabetu, kunena zoona, ndi mlongo wangadi ameneyu, chifukwa ndi mwana wa bambo wanga, koma osati womubala mai wanga, ineyo nkumukwatira. 13Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ” 14Tsono Abimeleki adabwezera Sara kwa Abrahamu, ndipo nthaŵi yomweyo adampatsa nkhosa, ng'ombe ndi akapolo aamuna ndi aakazi. 15Adauza Abrahamu kuti, “Dziko lonseli ndi langa, ungathe kukhala kulikonse komwe ukufuna.” 16Ndipo adauza Sara kuti, “Mlongo wakoyu ndikumpatsa ndalama zasiliva chikwi chimodzi, kuti zikhale ngati mboni kwa onse amene ali nawoŵa kuti iwe ndiwe wosalakwa.” 17Motero Abrahamu adapempherera Abimeleki, ndipo Mulungu adamchiza. Adachizanso mkazi wake pamodzi ndi antchito ake aakazi, kuti onsewo azitha kubala. 18Ndiye kuti Chauta anali ataŵatseka akazi onse a m'banja la Abimeleki kuti akhale osabala, chifukwa cha Sara mdzakazi wa Abrahamu.
Aktualisht i përzgjedhur:
Gen. 20: BLY-DC
Thekso
Ndaje
Copy
A doni që theksimet tuaja të jenë të ruajtura në të gjitha pajisjet që keni? Regjistrohu ose hyr
Bible Society of Malawi