Logoja YouVersion
Ikona e kërkimit

Gen. 13

13
Abramu ndi Loti asiyana
1Abramu ndi mkazi wake atachoka ku Ejipito, adapita ku Negebu, chigawo chakumwera. Ndipo Loti adapita nawo limodzi.
2Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe. 3Kuchokera kumwera adasendera ndithu cha ku Betele, ku malo aja kumene kale adaamangako hema lake, pakati pa Betele ndi Ai. 4Tsono adabwereranso ku malo aja kumene kale adaamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba. 5Loti nayenso amene ankayenda limodzi ndi Abramu, anali ndi nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe pamodzi ndi banja lake ndi antchito ake amene ankakhala naye limodzi. 6Tsono dziko lodyetsapo zoŵeta linali losakwanira onse aŵiriwo, poti aliyense anali ndi zoŵeta zambiri. 7Motero padaauka ndeu pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthaŵi imeneyo nkuti Akanani ndi Aperizi akadalipo m'dzikomo.
8Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga. 9Tiye tisiyane, usankhe dera lina lililonse la dziko lino limene ufuna. Iwe ukapita kwina, inenso ndipita kwina.” 10#Gen. 2.10 Motero Loti atayang'anayang'ana, adaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yordani mpaka ku Zowari chili ndi madzi ambiri. Chigwacho chinali ngati munda wa Chauta#13.10: Munda wa Chauta: Mau ameneŵa anena “Munda wa Edeni”. kapenanso ngati dziko la Ejipito. Nthaŵi imeneyi nkuti Chauta asanaononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora. 11Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana. 12Abramu adakhala m'dziko la Kanani, koma Loti adakhazikika pakati pa mizinda yam'chigwa, nakamanga hema pafupi ndi mzinda wa Sodomu. 13Anthu amumzindawo anali oipa kwambiri, ndipo ankachimwira Chauta.
Abramu asendera ku Hebroni
14Loti atachoka, Chauta adauza Abramu kuti, “Uyang'ane bwino kumpoto, kumwera, kuvuma ndi kuzambwe. 15#Ntc. 7.5 Ndidzakupatsa dziko lonse limene ukuliwonalo, iweyo pamodzi ndi zidzukulu zako. Ndipo lidzakhala lako mpaka muyaya. 16Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kudzaziŵerenga. Yekhayo amene angaŵerenge fumbi la pa dziko lapansi, ndiye adzathe kuŵerenga zidzukulu zakozo. 17Nyamuka tsopano, uyendere dziko lonselo, chifukwa ndakupatsa,” 18Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa.

Aktualisht i përzgjedhur:

Gen. 13: BLY-DC

Thekso

Ndaje

Copy

None

A doni që theksimet tuaja të jenë të ruajtura në të gjitha pajisjet që keni? Regjistrohu ose hyr