Yoh. 9
9
Yesu achiritsa munthu wakhungu
1Pamene Yesu ankayenda, adaona munthu wa khungu lobadwa nalo. 2Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” 3Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye. 4Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito. 5#Mt. 5.14; Yoh. 8.12Pamene ndili pansi pano, ndine kuŵala kounikira anthu onse.”
6Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo, 7namuuza kuti, “Pita ukasambe ku dziŵe la Siloamu.”#9.7: Dziŵe la Siloamu: Ndi dziŵe lina lake ku Yerusalemu. Ndilo lija akulitchula pa 2 Maf. 20.20; 2 Mb. 32.30. (Tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, Wotumidwa.) Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya.
8Pamenepo anzake ndi anthu amene kale ankamuwona akupemphapempha adati, “Kodi uyu si uja ankakhala pansi apa nkumangopempha?” 9Ena adati, “Ndiye amene.” Ena nkumati, “Iyai, akungofanafana naye.” Koma mwiniwakeyo adati, “Ai ndithu, ndine amene.” 10Apo anthu aja adamufunsa kuti, “Nanga maso ako apenya bwanji?” 11Iyeyo adati, “Munthu uja amati Yesuyu anakanda thope nalipaka m'maso mwangamu. Kenaka anandiwuza kuti, ‘Pita, ukasambe ku Siloamu. Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamba kupenya.’ ” 12Anthuwo adamufunsa kuti, “Iyeyo ali kuti?” Munthu uja adati, “Kaya, sindikudziŵa.”
Afarisi amufunsitsa munthu wochiritsidwayo
13Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi. 14Tsiku limene Yesu adaakanda thope namchiritsalo linali la Sabata. 15Tsono Afarisi nawonso adamufunsa munthu uja kuti, “Iwe, wapenya bwanji?” Iye adaŵauza kuti, “Anandipaka thope m'maso mwanga, ine nkukasamba, ndipo tsopano ndikupenya.” 16Afarisi ena adati, “Munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhudza tsiku la Sabata.” Koma ena adati, “Kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana.
17Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.” 18Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake. 19Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, uyu ndi mwana wanu? Ndiye mukuti adaabadwadi wosapenya? Nanga zatani kuti tsopano akupenya?” 20Makolo ake adati, “Chimene tikudziŵa ife nchakuti ameneyu ndi mwana wathu, ndipo adaabadwadi wosapenya. 21Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziŵa m'mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziŵanso. Mufunseni mwiniwakeyu, ngwamkulu, afotokoze yekha.” 22Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo. 23Nchifukwa chake makolo akewo adati, “Ngwamkulu, mufunseni mwiniwakeyu.”
24Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiŵiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziŵa kuti munthu amene uja ngwochimwa.” 25Iye adati, “Zakuti Iye ngwochimwa, ine sindikudziŵa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziŵa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.” 26Iwo adamufunsa kuti, “Kodi anachita chiyani pamene anakupenyetsa?” 27Iye adati, “Ndakuuzani kale, koma simumasamalako. Nanga chifukwa chiyani mukufuna kuzimvanso? Kapenatu nanunso mukufuna kukhala ophunzira ake eti?” 28Pamenepo iwo adayamba kumlalatira, adati, “Wophunzira wake ndi iweyo. Ife ndifetu ophunzira a Mose. 29Tikudziŵa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose, koma uyu sitikudziŵa kumene wachokera.” 30Munthuyo adati, “Pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziŵa kumene Iye wachokera, komabe wandipenyetsa. 31Timadziŵa kuti Mulungu samvera anthu ochimwa. Koma munthu akasamala za Mulungu, nachita zimene Mulungu afuna, Mulungu amamumvera. 32Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu. 33Munthu ameneyu akadapanda kuchokera kwa Mulungu, sakadatha konse kuchita kanthu.” 34Iwo adati, “Iwe udabadwa m'machimo okhaokha. Ndiye iweyo nkutiphunzitsa ife?” Atatero adamtulutsa nkumudula ku mpingo.
Za kusapenya kwamumtima
35Yesu adamva kuti Ayuda amtulutsa ndi kumdula ku mpingo munthu uja. Tsono pamene adampeza, adamufunsa kuti, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?” 36Iye adati, “Ambuye, mundiwuzetu ndani Iyeyo, kuti ndimkhulupirire.” 37Yesu adamuuza kuti, “Wamuwona kale, ndi yemwe akulankhula nawe.” 38Iye adati, “Ambuye, ndikukhulupirira.” Atatero adamgwadira.
39Tsono Yesu adati, “Ndidabwera pansi pano kudzaweruza, kuti osapenya apenye, ndipo openya achite khungu.” 40Afarisi ena amene anali pafupi naye, atamva zimenezi adamufunsa kuti, “Kodi monga ifenso ndife akhungu?” 41Yesu adati, “Mukadakhala akhungu, bwenzi mulibe mlandu. Koma chifukwa mukuti, ‘Tikupenya,’ ndiye kuti mlandu wanu ulipobe.”
Currently Selected:
Yoh. 9: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi