YouVersion Logo
Search Icon

Yoh. 20

20
Yesu auka kwa akufa
(Mt. 28.1-10; Mk. 16.1-8; Lk. 24.1-12)
1Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. 2Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” 3Pamenepo Petro ndi wophunzira wina uja adatuluka napita ku manda. 4Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. 5Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo. 6Simoni Petro atafika akumutsatira, adaloŵa m'mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, 7ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. 8Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. 9Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa. 10Pambuyo pake ophunzirawo adabwerera kwao.
Yesu aonekera Maria wa ku Magadala
(Mk. 16.9-11)
11Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo, 12naona angelo aŵiri ovala zovala zoyera. Angelowo adaakhala pansi, wina kumutu, wina kumapazi pamalo pamene padaagona mtembo wa Yesu paja. 13Iwo adamufunsa kuti, “Inu mai, mukuliranji?” Iye adati, “Chifukwa aŵachotsa Ambuye anga ndipo sindikudziŵa kumene akaŵaika.” 14Atanena zimenezi adacheuka, naona Yesu ataimirira pomwepo, koma sadamzindikire kuti ndi Yesu. 15Tsono Yesu adamufunsa kuti, “Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani?” Maria ankayesa kuti ndi wakumundako, motero adamuuza kuti, “Bambo, ngati mwaŵachotsa ndinu, mundiwuze kumene mwakaŵaika, kuti ndikaŵatenge.” 16Yesu adati, “Maria!” Iye adacheuka, nanena kuti, “Raboni!” (Ndiye kuti “Aphunzitsi” pa chihebri) 17Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ ” 18Maria wa ku Magadalayo adapita, nakauza ophunzira aja kuti, “Ndaŵaona Ambuye,” ndipo adaŵakambira zimene Ambuyewo adaamtuma.
Yesu aonekera ophunzira ake
(Mt. 28.16-20; Mk. 16.14-18; Lk. 24.36-49)
19Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” 20Atatero, adaŵaonetsa manja ake ndi m'nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri poŵaona Ambuyewo. 21Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” 22Pambuyo pake adaŵauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. 23#Mt. 16.19; 18.18Anthu amene mudzaŵakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzaŵakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”
Za kusakhulupirira kwa Tomasi
24Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. 25Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife taŵaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “Ndikapanda kuwona mabala a misomali m'manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m'nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.”
26Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m'nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” 27Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” 28Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” 29Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.”
Cholinga cha bukuli
30Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m'buku muno. 31Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m'dzina lake.

Currently Selected:

Yoh. 20: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in