Yoh. 14
14
Yesu ndiye njira ya kwa Atate
1Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. 2M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. 3Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine. 4Ndipo kumene ndikupita Ineko, njira yake mukuidziŵa.”
5Tomasi adati, “Ambuye, sitikudziŵa kumene mukupita, nanga njira yake tingaidziŵe bwanji?” 6#Bar. 3.13, 14Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine. 7Mukadandidziŵa Ine, Atate anganso mukadaŵadziŵa. Kuyambira tsopano mukuŵadziŵa ndipo mwaŵaona.”
8Filipo adati, “Ambuye, tiwonetseni Atatewo, mukatero tikhutira.” 9Yesu adamuyankha kuti, “Iwe Filipo, ndakhala nanu nthaŵi yonseyi, ndipo sunandidziŵebe? Amene waona Ine, waonanso Atate. Nanga bwanji ukuti, ‘Tiwonetseni Atate?’ 10Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. 11Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. 12Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Lonjezo la Mzimu Woyera
15 #
Lun. 6.18
“Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. 16Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. 17Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. 18Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. 19Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu.
21 #
Lun. 6.12, 18; Mphu. 4.14 “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
22Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” 23Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. 24Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.
25“Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. 26Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
27“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. 28Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. 29Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. 30Sindilankhula nanunso zambiri tsopano ai, pakuti Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lapansi, alikudza. Iyeyo alibe mphamvu pa Ine, 31koma anthu onse ayenera kudziŵa kuti ndimakonda Atate, nchifukwa chake ndikuchita monga Atate adandilamulira. Tiyeni, tizipita.”
Currently Selected:
Yoh. 14: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi