Ntc. 3
3
Petro achiritsa munthu wopunduka miyendo
1Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu pa 3 koloko madzulo, nthaŵi ya mapemphero. 2Anthu ena adaanyamula munthu wina wopunduka miyendo chibadwire. Masiku onse ankamuika pa khomo la Nyumba ya Mulungu lotchedwa “Khomo Lokongola,”#3.2: Khomo Lokongola: Limeneli linali khomo la Nyumba ya Mulungu lakuvuma. kuti iye azipempha kwa anthu oloŵa m'Nyumbamo. 3Pamene iye adaona Petro ndi Yohane akuloŵa m'Nyumba ya Mulungu, adaŵapempha kuti ampatseko kanthu. 4Iwo adampenyetsetsa, ndipo Petro adamuuza kuti, “Tatiyang'ana” 5Iye nkuŵayang'anadi namaganiza kuti alandira kanthu kwa iwo. 6Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!” 7Atatero adamgwira dzanja lamanja, namuimiritsa. Pompo mapazi ake ndi akakolo ake adalimba. 8Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu. 9Anthu onse adamuwona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10Adamzindikira kuti ndi yemwe uja amene ankakhala pa Khomo Lokongola la Nyumba ya Mulungu. Ndipo adazizwa ndithu ndi kudabwa ndi zimene zidamchitikira.
Mau a Petro m'Nyumba ya Mulungu
11Munthu uja adaakangamira Petro ndi Yohane, ndipo anthu onse adadabwa, naŵathamangira ku Khonde lotchedwa Khonde la Solomoni.#3.11: Khonde la Solomoni: Ndi khonde la Nyumba ya Mulungu lakuvuma (onani Yoh. 10.23.) Pambuyo pake akhristu ankasonkhana m'menemo (Ntc. 5.12.). 12Pamene Petro adaona zimenezi, adalankhula nawo anthuwo, adati, “Inu Aisraele, bwanji mukuzizwa ndi zimenezi? Bwanji mukutiyang'ana ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu zathuzathu? Kodi mukuyesa kuti nchifukwa choti ndife opembedza Mulungu kopambana? 13#Eks. 3.15Iyai, koma Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adapereka ulemerero kwa Yesu, Mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula. 14#Mt. 27.15-23; Mk. 15.6-14; Lk. 23.13-23; Yoh. 19.12-15Yesu anali woyera mtima ndi wolungama, koma inu mudamkana, ndipo m'malo mwake mudapempha kuti akumasulireni chigaŵenga. 15Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16Munthuyu, amene mukumuwona ndipo mukumdziŵa, wakhulupirira dzina la Yesu. Chikhulupirirocho chimene ali nacho mwa Yesu, ndicho chalimbitsa miyendo yake, chamchiritsa kwenikweni, monga inu nonse mukuwoneramu.
17“Ndiponso tsopano abale anga, ndikudziŵa kuti inu ndi akuluakulu anu mudachita zimenezi mosadziŵa. 18Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti Wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo zidachitikadi momwemo. 19Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo, 20ndipo adzakutumizirani Yesu uja amene adamusankhuliratu kuti akhale Mpulumutsi wanu. 21Iyeyo anayenera kukhala Kumwamba mpaka nthaŵi yakukonza zonse kwatsopano, monga Mulungu adanenera kuyambira kalekale mwa aneneri ake oyera mtima. 22#Deut. 18.15, 18 Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni. 23#Deut. 18.19Aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, amchotseretu mwa Aisraele ndi kumuwononga.’ 24Ndipo aneneri onse amene adalankhula, kuyambira Samuele, mpaka onse amene adadza pambuyo pake, ankalalika za masiku omwe ano. 25#Gen. 22.18 Zimene Mulungu adalonjeza kudzera mwa aneneri nzokhudza inuyo ana ao. Momwemonso chipangano chimene adachita ndi makolo anu chikukhudza inu ana ake. Paja adauza Abrahamu kuti, ‘Mwa chidzukulu chako china ndidzadalitsa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi.’ 26Choncho Mulungu atasankhula Mtumiki wake adayamba kumtuma kwa inu, kuti akudalitseni pakuthandiza aliyense mwa inu kusiya njira zake zoipa.”
දැනට තෝරාගෙන ඇත:
Ntc. 3: BLY-DC
සළකුණු කරන්න
බෙදාගන්න
පිටපත් කරන්න
ඔබගේ සියලු උපාංග හරහා ඔබගේ සළකුණු කල පද වෙත ප්රවේශ වීමට අවශ්යද? ලියාපදිංචි වී නව ගිණුමක් සාදන්න හෝ ඔබගේ ගිණුමට ඔබගේ ගිණුමට පිවිසෙන්න
Bible Society of Malawi