YouVersion Logo
Search Icon

Yohane 2

2
Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
1Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, 2ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. 3Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”
Iwo anachita momwemo. 9Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu
12Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
13Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. 15Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. 16Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
17Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
18Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
19Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
20Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?” 21Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake. 22Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
23Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake. 24Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse. 25Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.

Currently Selected:

Yohane 2: CCL

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in