Gen. 9
9
Chipangano cha Mulungu ndi Nowa
1 #
Gen. 1.28
Mulungu adadalitsa Nowa ndi ana ake omwe, nati “Mubale ana ambiri ndi kuchulukana, kuti mudzaze dziko lonse lapansi. 2Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule. 3Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu. 4#Lev. 7.26, 27; 17.10-14; 19.26; Deut. 12.16, 23; 15.23 Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake. 5Aliyense wopha munthu, adzaphedwa. Nyama iliyonse yopha munthu, idzaphedwa. Munthu aliyense wopha mnzake, iyenso aphedwe.
6 #
Eks. 20.13; Gen. 1.26 “Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa,
pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
7 #
Gen. 1.28
Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.”
8Mulungu adauza Nowa ndi ana ake kuti, 9“Tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, 10ndi zamoyo zonse, mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m'chombo. 11Chipanganocho ndi ichi: ‘Ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ ”
12Ndipo Mulungu adati, “Nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu. 13Ndikuika utawaleza m'mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi. 14Nthaŵi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga, ndipo pakaoneka utawaleza m'mitambomo, 15ndizidzakumbukira lonjezo langa limene ndidachita ndi inu ndi nyama zonse, kuti chigumula chisadzaonongenso zamoyo zonse. 16Utawaleza ukamadzaoneka m'mitambo, Ine ndidzaupenya, ndipo ndizidzakumbukira chipangano chamuyaya cha pakati pa Ine ndi zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi. 17Chimenechi ndi chizindikiro cha chipangano chimene ndachita ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.”
Nowa ndi ana ake
18Ana a Nowa omwe adatuluka m'chombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu ndiye anali bambo wa Kanani. 19Ana a Nowa atatu ameneŵa ndiwo makolo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
20Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa. 21Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake. 22Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja. 23Koma Semu ndi Yafeti adatenga chofunda nachiika kumbuyo kwao, atachinyamula pa mapewa. Tsono adayenda chafutambuyo nafunditsa bambo wao. Sadapenyeko kumene kunali bambo wao uja ndipo sadaone maliseche ake. 24Nowa atadzuka, adamva zonse zimene mwana wake wamng'onoyo adaachita, 25ndipo adati,
“Atembereredwe Kanani!
Adzakhala kapolo weniweni wa abale ake.”
Popitiriza mau adati,
26“Atamandike Chauta, Mulungu wa Semu,
Kanani adzakhale kapolo wa Semuyo.
27Mulungu amkuze Yafeti.
Zidzukulu zake zidzagaŵane madalitso
ndi zidzukulu za Semu.
Kanani adzakhale kapolo wa Yafetiyo.”
28Chitatha chigumulacho, Nowa adakhala ndi moyo zaka zina 350. 29Adamwalira ali wa zaka 950.
Atualmente selecionado:
Gen. 9: BLY-DC
Destaque
Partilhar
Copiar
Quer salvar os seus destaques em todos os seus dispositivos? Faça o seu registo ou inicie sessão
Bible Society of Malawi