1
YOHANE 13:34-35
Buku Lopatulika
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.
ႏွိုင္းယွဥ္
YOHANE 13:34-35ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
2
YOHANE 13:14-15
Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.
YOHANE 13:14-15ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
3
YOHANE 13:7
Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake.
YOHANE 13:7ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
4
YOHANE 13:16
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye.
YOHANE 13:16ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
5
YOHANE 13:17
Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.
YOHANE 13:17ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
6
YOHANE 13:4-5
ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m'mene adatenga chopukutira, anadzimanga m'chuuno. Pomwepo anathira madzi m'beseni, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.
YOHANE 13:4-5ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
ပင္မစာမ်က္ႏွာ
က်မ္းစာ
အစီအစဥ္
ဗီဒီယို