YOHANE 9
9
Achiritsidwa munthu wosaona chibadwire
1Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire. 2Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona? 3#Yoh. 11.4Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye. 4#Yoh. 4.34; 17.4Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito. 5#Yoh. 12.35-36, 46Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndili kuunika kwa dziko lapansi. 6#Mrk. 7.33; 8.23Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso, 7#Neh. 3.15; 2Maf. 5.15nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona. 8Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha? 9Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene. 10Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji? 11#Yoh. 8.6-7Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya. 12Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.
13Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi. 14Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ake. 15Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya. 16#Mat. 12.2; Yoh. 8.33Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo. 17#Yoh. 6.14Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri. 18Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya; 19nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona? 20Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wake ndi amake anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona; 21koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha. 22#Yoh. 7.13; 8.34Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge. 23Chifukwa cha ichi atate wake ndi amake anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye. 24Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa. 25Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya. 26Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji? 27Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala ophunzira ake? 28Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife ophunzira a Iyeyu, ife ndife ophunzira a Mose. 29#Yoh. 8.14Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo. 30Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga. 31#Mas. 66.18; Yer. 11.11; Mik. 3.4Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo. 32Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire. 33#Yoh. 3.2Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu. 34Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.
35 #
Mat. 16.15-16
Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Munthu? 36Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye? 37#Yoh. 4.26Yesu anati kwa iye, Wamuona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo. 38Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira Iye. 39#Yoh. 5.22, 27Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona. 40Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye anamva izi, nati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osaona? 41#Yoh. 15.22, 24Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.
सध्या निवडलेले:
YOHANE 9: BLPB2014
ठळक
सामायिक करा
कॉपी करा
तुमचे हायलाइट तुमच्या सर्व डिव्हाइसेसवर सेव्ह करायचे आहेत? साइन अप किंवा साइन इन
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi